Chilimikani polimbana ndi HIV!

Kodi kafukufuku wa katemera ndi chiyani?

Chitetezo chanu cham’thupi chimakutetezani ku matenda. Katemera amaphunzitsa thupi kuti lithe kuteteza kapena kulimbana ndi matenda ena ake. Popanga katemera akatsiwiri ofufuza amayenera kumuyeserera katemerayo mwa anthu. Kafukufuku wa katemera amayesa ngati katemerayo sangayambitse zovuta zina m’thupi la munthu (sayambitsa mavuto azaumoyo ) komanso kuonangati chitetezo cha m’thupi la munthu chikutha  kugwilizana ndi katemera wa m’kafukufukuyu. Kafukufuku wa katemera amathanso kugwira ntchito yowona ngati katemera angateteze kapena kulimbana ndi matenda odziwika. Pamayenera kuchitika akafukufuku wochuluka kuti papezeke katemera wopanda vuto lina lilonse m’thupi komanso wothandiza kwambiri. 

Kodi umoyo ndi maufulu wa otenga nawo mbali m mukafukufuku udzatetezedwa bwanji?

Kuteteza thanzi ndi kulemekeza ufulu wa otenga nawo mbali ndi zofunikira kambiri kwa aliyese   ku bungwelofufuza zakatemela wa HIV (HIV Vaccine Trials Network) ndi aku Janssen Vaccines ndi mbali yo teteza B.V., imene ili thambi ya company yopanga mankhwala ya Johnson & Johnson. Ogwira ntchito kuchipatala cha kafukufuku adzafotokozera amene akufuna kutenga nawo mbali mu kafukufuku mwa tsatanetsataneza katemera wa  kafukufukuyu ndi ndondomeko zoyenera kutsata, phindu lake komanso zovuta zotenga nawo mbali mukafukufuku,  ndi ufulu umene angakhale nawo ngati otenga nawo mbali mukafukufuku. Komanso munthu ali ndi ufulu wovomera kapena kukana kutenga nawo mbali mukafukufukuyu – chiganizo cholowa kapena kukana ndi chainuyoPanthawi ya kafukufukuyu, ogwira ntchito pachipatala adzayang’anira anthu otenga nawo mbali mukafukufuku pofuna kuonetsetsa kuti katemerayu sakuyambitsa zovuta zina pa umoyo wawo. Achipatala adzafunsanso anthuwa ngati akukumana ndi zovuta pamoyo wawo chifukwa chotenganawo mbali mukafukufukuyu ndipo adzawathandiza kuthana ndi mavutowo.

 Palinso magulu angapo oyima paokha amene amagwira ntchito yoteteza ufulu ndi umoyo wa anthu amene akutenga nawo mbali mukafukufuku. Ngati mungakhale ndi chidwi chofuna  kudziwa zambiri, ogwira ntchito ku zipatala za kafukufuku zimene muli nazo pafupi adzakufotokozerani zambiri za maguluwa.