Za Imbokodo

Imbokodo ndi chiyani?

Imbokodo ndi kafukufuku wamkulu amene akuyeserera akatemera awiri ophatikizana pofuna kuona ngati angateteze kuHIV. Katemerayu akutchedwea Ad26.Mos4.HIV (katemera wa Ad26) ndi Clade C gp140 (katemera wa puloteni). Zolinga zazikulu za kafukufukuyu ndikufuna kudziwa izi:

  • Kodi katemera angateteze kutenga HIV?
  • Kodi katemerayu alibe vuto lina lililonse paumoyo wa munthu?
  • Kodi chitetezo cha m’thupi mwa anthu chingathe kugwira ntchito limodzi ndi katemera wa kafukufuku?

Katemera amene akuyesedwa mu kafukufuku uno SANGAYAMBITSE HIV kapena Edzi.Sanapangidwe kuchokera ku HIV yamoyo, HIV yakufa, kapena tidzidutswa ta HIV kapena tima cello tam’thupi la munthu amene ali ndi HIV. Ndizopangidwa mochita kuyerekeza kuti zizifanana ndi HIV motero kuti sizingayambitse HIV kapena Edzi. 

Katemera wa kafukufukuyu ndi wongoyeserera. Izi zikuthandauza kuti akumufufuzabe ndikupitiriza kuphunzira ngati alibe vuto lina lirironse tikamugwiritsa ntchito pa anthu komanso kufuna kudziwa ngati angateteze ku kachirombo ka HIV.

A katemerawa akugwiritsidwa ntchito pa zolinga za kafukufuku zokha basi. Sakupezeka kwa anthuaku madela ndipo siwogulitsa. Akupereka katemerayu ndi amene akumupanga, a Janssen Vaccines & Prevention B.V., nthambi ya Janssen Pharmaceutical Companies of Johnson & Johnson.

Tafotokozani zambiri za Imbokodo

Imbokodo is a large study that aims to prove that these vaccines can protect women in sub-Saharan Africa from HIV infection. If Imbokodo can show that these vaccines work in women in sub-Saharan Africa, it will be a very important step on the way to finding a safe and effective vaccine that will protect people around the world from HIV. 

Kafukufuku wina wamkulu amene anachitika m’chaka cha 2009, anasonyeza koyamba kuti katemera angathe kuteteza ku HIV ngakhale kuti chitetezo chake ndi chochepa. Kafukufuku ameneyu ankatchedwa RV144 ndipo anachitikira ku Thailand analemba anthu oposa 16000. Zotsatira zake zinali zosangalatsa, ndipo zinasonyeza kuti katemerayu anateteza anthu 31.2 mwa anthu 100 kuti asatengenso HIV. Izi zikutanthauza kuti katemera amene anagwiritsidwa ntchito mu kafukufuku wa RV144 anakwanitsa kuteteza pafupifupi munthu mmodzi mwa anthu atatu alionse kuti asatenge HIV pamene amatenga nawo mbali mukafukufuku. Ngakhale kuti zotsatirazi sizinali zokwanira kuti katemerayu apatsidwe chiphaso kuti anthu ayambe kumugwiritsa ntchito, anathandizabe akatswiri azascience kuti apeze zizindikiro ndi mfundo zofunikira kuti ziwathandize kupanga katemera wabwino. Katemera amene akuyesedwa mu kafukufuku wa Imbokodo ndi osiyana ndi amene anagwiritsidwa ntchito mu kafukufuku wa RV144. 

Katemera amene akugwiritsidwa ntchito mu Imbokodo komanso makatemera ena ofananako, anayesedwapo m’kafukufuku ena ocheperako. Imodzi mwa kafukufuku awangonowa ndi wotchedwa Approach, yemwe amagwiritsa ntchito katemera ofananako ndiwa Ad26 komanso katemera wa puloteni wofanana ndi wa mu Imbokodo ndipo akuchitikira ku US, Rwanda, Uganda, South Africa, ndi Thailand. Katemera wa Ad26 ndi katemera wa puloteni amene akugwiritsidwa ntchito mu kafukufuku wa Imbokodo akuperekedwanso kwa anthu 235 m’kafukufuku muwiri amene akuchitikira ku US, Kenya, ndi Rwanda ndipo akutchedwa HVTN 117 (Traverse) ndi HVTN 118 (Ascent). Kafukufuku wa Traverse ndi Ascent ali mu ndime yoyambirira yoyeserera ndipo akatsiwiri a kafukufuku akufuna kudziwa ngati katemera wa Ad26 ndi puloteni (katemera yemwe akugwiritsidwanso ntchito mu Imbokodo) alibe vuto lina lirironse pamoyo wa munthu; ngati anthu angathe kulandira katemera wa kafufufukuyu popanda kukumana ndi zovuta zina ziri zonse; momwe chitetezo cham’thupi chimagwirira ntchito ndi katemera wa Ad26 ndi wa puloteni. Zotsatira zoyambirira kuchokera ku kafukufuku wa Traverse, komanso kuchokera ku kafukufuku wa Approach yemwe tamufotokoza pamwambapa zikusonyeza kuti katemerayu alibe vuto lina lililonse atapelekedwa kwa munthu ndipo akutha kuchititsa kuti chitetezo cha m’thupi chigwire ntchito yake bwino.

Pa kafukfufku amene anapangidwa m’mbuyomu, palibe mavuto akulu azaumoyo amene anadza kaamba ka katemerayu. Komabe, ndizotheka kuti pakhale mavuto ena amene pakadali pano sitinawaone. Ichi ndi chifukwa chake chimodzi cha zolinga za kafukufuku uno ndi kufuna kuona ngati katemerayu sangayambitse vuto lina lirironse ataperekedwa kwa anthu.Umoyo waaliyense amene akutenga nawo mbali mukafukufuku udzaunikidwa pa nthawi yonse ya kafukfukuyu.

Kafukufuku wa Imbokodo akusiyana ndi akafukufuku ena angono angono,pakuti mu kafukufuku wa Imbokodo, akatswiri a kafukufuku tsopano akufuna aphunuzirepo ngati katemera wa Ad26 ndi wa puloteni angathedi kuteteza kuHIV. 

Ndani akuchita kafukufukuyu?

Kafukufukuyu akuyendetsedwa ndi a HVTN, Janssen Vaccines & Prevention B.V., nthambi ya Janssen Pharmaceutical Companies ya Johnson & Johnson, pamodzi ndi zipatala zonse zimene zikuchita nawo kafukfufkuyu. Magulu amenewa akugwira ntchito mothandizana ndi anthu ndi mabungwepofuna kuonetsetsa kuti kafukufukuyu ndi wovomerezeka m’deralo komanso kuti akulemekeza zikhalidwe zam’deralo.