1. Kodi kafukufuku wa katemera ndi chiyani?

Katemera amaphunzitsa thupi kuti lizitha kudziteteza kapena kulimbana ndi matenda ena ake. Kuti katemera apangidwe, akatswiri a kafukufuku amayenera kumuyeserera katemerayo mwa anthu. Kafukufuku wina wa katemera amakhala wofuna kuona ngati katemerayo sangayambitse zovuta zina m’thupi la munthu (sayambitsa matenda) komanso kuona ngati chitetezo cha m’thupi la munthu chikutha kulimbana ndi katemera wa kafukufukuyu. Chitetezo cha m’thupi mwanu chimakutetezani ku matenda. Kafukufuku wina wa katemera amathandizanso kudziwa ngati katemera angateteze kapena kulimbana ndi matenda. Pamayenera kuchitika kafukufuku wochuluka kuti papezeke katemera wopanda vuto lilonse m’thupi komanso wothandiza kwambiri.

Pakadali pano palibe katemera wovomerezeka wa HIV kapena Edzi.

2. Kodi kafukufuku wa Kafukufuku wa Katemera wa HVTN 705/HPX2008 ndi chiyani?

Kafukufuku wa Katemera wa HVTN 705/HPX2008 akuyesa katemera muwiri wa HIV. Katemera wa kafukufukuyu akutchedwa Ad26.Mos4.HIV ndi Clade C gp140. Katemera ameneyu anapangidwa ndi kampani ya Janssen Vaccines & Prevention B.V. Kuyambira pano mpaka m’tsogolo m’kabuku kano katemerayu tizingomutchula katemera wa Ad26 ndi Poloteni kapena katemera wa kafukufuku.

Katemera wa Ad26

Katemera wa Ad26 amapangidwa kuchokera ku vayilasi yotchedwa Adenovirus type 26. Mu katemerayu amayikamo tizigawo tina ta HIV. Cholinga chake ndikuti azitha kuliwuza thupi kuti lipange mapoloteni ofanana ndi amene amapezeka mu HIV. (Mapoloteni ndi timagawo tachilengedwe tam’thupi timene timapezeka m’zinthu zonse zamoyo, monga m’thupi la munthu komanso m’mavayirasi monga HIV). Chitetezo cham’thupi chimalimbana ndi mapoloteni a HIV ongoyerekeza amene amayikidwa m’katemera wa kafukufuku. Apa ndiye kuti chitetezo cham’thupi chikulimbana ndi matenda. Pamene chitetezo cham’thupi chikulimbana ndi matenda thupi limakonzeka kuti lizitha kuzindikira mapoloteni omwewo amene ali mu HIV ndikulimbana ndi kachiromboka ngati munthu atadzatenga HIV patsogolo. Tizirombo ta vayirasi ya Adenovirus 26 nditodziwika bwino kwambiri pamoyo watsiku ndi tsiku ndipo timayambitsa chimfine komanso vuto la mapumidwe. Koma adenovirus amene tikumugwiritsa ntchito mu katemera wa kafukufukufu uno tamufowoketsako pang’ono kuti asayambitse matenda ndipo sangayambitse vuto lina lililonse mwa anthu.

Katemera wa Poloteni

Katemera wa poloteni wotchedwa Clade C gp140, amapangidwa kuchokera ku mapoloteni ofanana ndi mapoloteni amene amapezeka pamwamba pa HIV. Katemera ameneyu angathandize kupanga chitetezo cha m’thupi.

Katemera wa mapoloteni amene akugwiritsidwa ntchito mu kafukufukuyu amapahtikizidwa ndi mankhwala owonjezera otchedwa Aluminum Phosphate. Mankhwala owonjezerawa ndi mankhwala amene amaphatikizidwa ku katemera pofuna kuwonjezera mphamvu ya chitetezo polimbana ndi matenda. Aluminium amagwiritsidwa ntchito m’katemera wambiri monga wa Hepatitis A ndi B, diphtheria, ndi kafumbata.

Mankhwala amene tikugwiritsa ntchito mu kafukufukuyu sanapangidwe kuchokera ku HIV yamoyo, HIV yakufa, kapena timinofu tam’thupi la munthu amene li ndi HIV. Katemera wa kafukufukuyu sangayambitse HIV kapena Edzi.

Mukafuna kumva zambiri za katemera wa kafukufukuyu titha kukufotokozerani.

3. Ndi mabungwe ati amene akuchita kafukufukuyu?

Bungwe lowona za matenda a ziwengo komanso matenda opatsirana la National Institute of Allergy and Infectious Diseases (NIAID), Gulu la mabungwe oyeserera katemera la HIV Vaccine Trials Network (HVTN) ndi kampani ya Janssen Vaccines and Prevention B.V ndi amene anakonza kafukufukuyu. Kampani ya Janssen Vaccines & Prevention B.V ndi imene imapereka chithandizo komanso ndi yomwe ikupereka katemera. Bungwe la NIAID ndi nthambi ya mabungwe a zaumoyo la National Institutes of Health (NIH) yomwe ndi gawo la Boma la United States.

Mabungwe a HVTN ndi mgwirizano wa akatswiri a zasayansi, akatswiri a zamaphunziro komanso anthu wamba amene akusakasaka katemera wabwino wotetezera HIV. HVTN imalandira thandizo la ndalama kuchokera ku NIAID ndipo kafukufuku uyu akuthandizidwanso ndi bungwe la Bill and Melinda Gates Foundation ndi Janssen Vaccines & Prevention B.V.

4. Kafukufukuyu adzachitika liti ndipo adzachitikira kuti?

Kafukufukuyu akuyembekezera kulemba anthu ochita nawo m’mwezi wa October, 2017 ndipo adzachitikira m’malo awa: 

 • Malawi: Lilongwe
 • Mozambique: Maputo
 • South Africa: Bloemfontein, Brits, Cape Town (Emavundleni, Khayelitsha, ndi Masiphumelele), Durban (Chatsworth, eThekwini, Isipingo, Tongaat ndi Verulam), Elansdoorn, Klerksdorp, Ladysmith, Mamelodi, Medunsa, Mthatha, Rustenburg, Soshanguve, Soweto (Bara ndi Kliptown), ndi Tembisa
 • Zambia: Lusaka and Ndola
 • Zimbabwe: Harare

5. Ndi chifukwa chiyani kafukufukuyu akuchitika?

Cholinga cha ntchito ya kafukufuku wa HVTN ndikupeza katemera wa HIV yemwe ndi wothandiza ndi wopanda vuto lina lililonse. Zolinga zenizeni za kafukufukuyu ndi:

 • Kuyesera ngati anthu sangatenge HIV atalandira katemera wa kafukufukuyu
 • Kufuna kudziwa zambiri ngati katemerayu alibe zovuta zina zilizonse pathupi la munthu
 • Kuti tidziwe momwe katemerayu angagwirire ntchito yoteteza kutenga HIV. 

6. M’kafukufukuyu mudzakhala anthu angati, ndipo ndani angalowe nawo?

M’kafukufukuyu mudzakhala amayi okwana 2600.

Kuti mayi alowe nawo m’kafukufukuyu ayenera kukhala wathanzi, wa zaka za pakati pa 18 ndi 35 ndipo kuti alibe HIV. Akhale akuti sangatenge pakati komanso asakhale kuti akuyamwitsa mwana. Komanso pali njira zina zosankhira. Tidzafunsa amayi za mbiri ya umoyo wawo, kuwawunika ndikutenga magazi komanso mkodzo kuti tikayeze. Tidzawafunsanso anthu onse za moyo wawo wogonana komanso ngati amagwiritsa ntchito mankhwala ozunguza ubongo. 

7. Kodi katemerayu siwoopsa?

Sitikudziwa zoopsa zonse za katemerayu chifukwa anangoperekedwako kwa anthu ochepa m’mbuyomu. Katemera wa poloteniyu anaperekedwa kwa anthu 300 ndipo wa Ad26 anaperekedwa kwa anthu 110. Ngakhale kuti m’mbuyomu palibe amene anakumanapo ndi vuto lina lililonse lodetsa nkhawa pa katemera wakafukufukuyu, n’kutheka kuti patha kupezeka zovuta zina zomwe sitimaziyembekezera. Ichi ndi chifukwa chake cholinga china cha kafukufukuyu ndikufuna kudziwa ngati katemerayu sangabweretse zovuta kwa anthu ngati ataperekedwa kwa anthu ochuluka. Munthu aliyense wochita nawo kafukufukuyu adzakhala akuyang’aniridwa ndi anamwino komanso madotolo panthawi yonse ya kafukufukuyu.

8. Kodi katemera wa kafukufukuyu angateteze ochita nawo kafukufukuyu kuti asatenge HIV?

Ochita nawo kafukufukuyu asaganize kuti angatetezedwe ku HIV chifukwa cha katemerayu. Choyenera kudziwa ndi chakuti anthu ena sadzalandira katemera m’ kafukufukuyu, chifukwa chakuti theka la anthuwa lidzalandira katemera wongoyerekeza (placebo). Placebo m’kafukufukuyu ndi madzi amchere owiritsidwa.

Cholinga cha kafukufukuyu ndi kufuna kudziwa ngati katemerayu angateteze kapena kulimbana ndi HIV.

Chifukwa chakuti sitikudziwa ngati katemerayu angateteze HIV/Edzi, ochita nawo kafukufukuyu adzapatsidwa uphungu pa kapewedwe ka HIV ndipo tidzawafotokozera za zipatala zimene angakapezeko njira zopewera kutenga HIV.

9. Zidzatenga nthawi yaitali bwanji kuti tidziwe ngati katemerayu ndi wothandizadi?

Tikuyembekeza kuti tidzatenga zaka 4 kuti tidziwe ngati katemerayu akutetezadi HIV. Ndizothekanso kuti titha kudziwa zotsatirazi mofulumilirako.

10. Kodi mudzateteza bwanji umoyo komanso ufulu wa anthu ochita nawo kafukufukuyu?

Kuteteza umoyo ndi kulemekeza ufulu wa anthu ochita nawo kafukufuku ndi zinthu zimene aliyense ku HVTN ndi Janssen Vaccines amaziyikira kumtima kwambiri pochita kafukufuku. Sitingathe kupeza katemera wa HIV popanda anthu odzipereka kuchita nawo kafukufukuyu.

Njira yoyamba pofuna kuteteza ufulu wa anthu ochita nawo kafukufuku ndikuwafotokozera zonse zokhudza kafukufukuyu asanalowe. Ogwira ntchito m’zipatala za kafukufukuyu adzafotokozera anthu za katemerayu, dongosolo loyenera kutsata mu kafukufukuyu, kuopsa kwake komanso ubwino wake kwa iwowo komanso za ufulu umene iwo ali nawo. Izi ndi monga kudziwitsidwa nkhani zatsopano zokhudza kafukufukuyu makamaka zinthu zimene zingawathandize kuchita chiganizo cholowa nawo kapena ayi, komanso za ufulu wotuluka mu kafukufukuyu nthawi ina iliyonse.

Panthawi ya kafukufukuyu, ogwira ntchito pachipatala cha kafukufuku adzayang’anira anthu ochita nawo kafukufuku pofuna kuonetsetsa kuti katemerayu sakuyambitsa zovuta zina pa umoyo wawo wa tsiku ndi tsiku. Achipatala adzafunsa anthuwa ngati akukumana ndi zovuta za pamoyo wawo chifukwa chochita nawo kafukufukuyu. Achipatalawa adzawathandiza wochita nawo kafukufuku ngati ali ndi vuto la zaumoyo kapena moyo wake wa tsiku ndi tsiku limene layamba chifukwa chochita nawo kafukufukuyu.

Palinso magulu angapo amene amagwira ntchito yoteteza ufulu ndi umoyo wa anthu amene akuchita nawo kafukufuku: 

 • Gulu la anthu amene amawunika ngati kafukufuku alibe vuto komanso pali gulu loyima palokha limene limachita kalondolondo wa kafukufukuyu. Maguluwa amaona dongosolo lofotokoza za kafukufukuyu kuti agamule ngati kafukufukuyo alibe vuto lina lililonse ndipo kuti athe kupitiriza kupereka majakisoni a kafukufuku.
 • Pa chipatala paliponse pamakhalanso komiti kapena gulu limene limaona ngati kafukufuku akutsatira ndondomeko la Instititutional Review Board a kapena Ethics Committee lomwe limawunika ndi kuchita kalondolondo wa ndondomeko ya momwe kafukufuku adzayendere, kuphatikizapo uthenga umene umapita kwa anthu kuwafotokozera za kafukufukuyu, momwe kafukufukuyu akuyendera komanso za mavuto a zaumoyo amene anthu akukumana nawo. Komitiyi imaonanso ngati ufulu wa anthu ochita nawo kafukufukuyu ukulemekezedwa.
 • Bungwe loyang’anira kagwiritsidwe ntchito ka mankhwala la South Africa Medicines Control Council, komanso mabungwe ena ogwira ntchito yomweyi m’mayiko amene mukuchitikira kafukufuku amayang’anira kayendetsedwe ka kafukufuku ndipo amayenera kulandira malipoti okhudza chitetezo cha anthu ochita nawo kafukufuku.
 • Bungwe la ku America loona za Chakudya ndi Mankhwala la US Food & Drug Administration (FDA) limawunikanso kafukufukuyu. Bungwe la FDA limaonetsetsa kuti kafukukufuku akutsatira malamulo a dziko okhudza kafukufuku wa anthu komanso pa kagwiritsidwe ntchito ka katemera mu kafukufuku.
 • Chipatala chilichonse cha kafukufuku chimakhala ndi Komiti Yoona Za Chitetezo cha anthu yotchewda Institutional Biosafety Committee (IBC) pa Chingelezi yomwe imayanga’nira momwe katemera wa kafukfuku akukonzedwera ku malo osungira mankhwala ndimomwe akumugwiritsira ntchito kuchipatala.
 • Zipatala zina zimakhala ndi makomiti apadera owona ngati kafukufuku akutsatira ndondomeko amene amayang’anira malo osungira magazi komanso zinthu zimene azitenga m’matupi a anthu. Malo amenewa amatchedwa mabanki osungirako ziwalo kapena zinthu za m’thupi.
 • Dipatimenti ya Zaulimi, Nkhalango ndi Usodzi m’dziko la South Africa ili ndi bodi yapadera imene imawunika ndi kuvomereza mapempho onse oyitanitsa kuchokera ku mayiko akunja zinthu zolengedwa mwamakono zomwe pa Chingelezi amati genetically modified materials (GMO). Katemera wa Ad26 amene akugwiritsidwa ntchito m’kafukufukuyu ndi chitsanzo cha zinthu za GMO.
 • Chipatala chilichonse cha kafukufuku chimakhala ndi Komiti kapena Bodi yam’dera yolangiza pantchito za kafukufuku. Mamembala ake amakhala anthu am’deralo amene amafotokozera ochititsa kafukufuku za madandaulo komanso zofuna za anthu am’deralo. Mamembala a komitiyi amakhala gawo la gulu limene likuchititsa kafukufuku. Amakonzanso kapena kuwunika uthenga wokafotokozera anthu amene akuchita nawo kafukufukuyu

11. Kodi kulandira katemera kungachititse kuti munthu awoneke ngati ali ndi HIV atayezetsa

Eya, ndizotheka kuti anthu amene akuchita nawo kafukufukuyu apezeke kuti ali ndi mitundu ina ya HIV atayezetsa. Ngati munthu walandira katemera wa HIV thupi lake limapanga asilikali olimbana ndi HIV. Asilikali amathandiza kulimbana ndi matenda. Kuyezetsa HIV ndi njira yofufuzira asilikali a HIV ngati chizindikiro chakuti munthu watenga matenda. Pachifukwachi, munthu atha kupezeka kuti ali ndi HIV ngakhale atakhala kuti sanatenge HIV. Izi ndi zotsatira zowoneka ngati uli ndi HIV chifukwa cha katemera. Zotsatira zimenezi pa Chingelezi amati vaccine-induced seropositive (VISP) kapena Vaccine-Induced Seroreactivity (VISR). Sitikudziwa ngati tidzakhale ndi zotsatira za mtunduwu ndipo kuti zotsatira zamtunduwu zingakhalepo kwa nthawi yaitali bwanji.

Anthu amene akayezedwa amapezeka kuti ali ndi HIV amafunika kuyezetsa kwapadera pofuna kutsimikiza ngati HIV ikupezeka chifukwa cha katemera kapena kuti ali nayodi. Zipatala zimene zokuchita nawo kafukufukuyu zili ndi zipangizo zoyezera zimene zimayang’ana kachirombo ka vayilasi m’malo moyang’ana asilikali. Anthu amene akuchita nawo kafukufukuyu akuyenera kukayezetsa ku zipatala zokhazo zimene zikuchita nawo kafukufukuyu.

Palibe vuto lina lililonse la zaumoyo lokhudzana ndi HIV yopezeka kamba ka katemera mukayezetsa koma zotsaira zokhazo zitha kuyambitsa mavuto m’magawo ambiri monga chisamaliro cha matenda kapena vuto la mano, kulembedwa ntchito, inshuransi, chiphaso cholowera mayiko ena, kapena kulowa ku usilikali. Anthu sangaloledwe kupereka magazi kapena ziwalo zina. Ngati anthu amene akuchita nawo kafukfuku akufuna kukhala ndi inshuransi, kulembedwa ntchito kapena usilikali ayenera kudziwitsa achipatala cha kafukufuku mwachangu. Kampani ya insutransi, olemba anthu ntchito kapena usilikali sangavomereze zotsatira za kuyezetsa ku HVTN. Koma HVTN itha kugwira nawo ntchito pofuna kuonetsetsa kuti pali ndi mwayi woyezetsa moyenera pofuna kudziwadi ngati muli ndi HIV kapena ayi. Ngati muli ndi asilikali am’thupi ndipo mwatenga pakati (mimba) mutha kumupatsira mwana womuyembekezerayo, ndipo mwanayo atayezetsa atha kumaonekanso ngati lai ndi HIV ndikuyamba kupatsidwa mankhwala. Achipatala cha kafukufuku adzakupatsani zotsatira za kuyezetsa kwanu zomwe mungagwiritse ntchito paliponse pamene zingafunike.

12. Ndingapeze kuti uthenga wina wokhudza kafukufukuyu?

Za kafukufuku wa katemera wa HIV: www.clinicaltrials.gov

Za mabungwe amene akuchita kafukufuku woyeserera katemera wa HIV: www.hvtn.org

Za zotsatira zosonyeza kuti munthu ali ndi HIV akayezetsa atalandira katemera: http://www.hvtn.org/VISP

Ngati muli ndi mafunso ena amene sitinathe kuwayankha pakufotokoza kwathuku, chonde tifunseni. Mutha kuyankhulana ndi: [email protected]