Odzipereka


Ndi anthu angati komanso ndani angatenge nawo mbali mukafukufukuyu?

Kafukufukfuyu adzalemba amayi pafupifupi 2600 a m’mayiko a South Africa, Malawi, Mozambique, Zambia, ndi Zimbabwe. Kuti amayi atenge nawo mbali m’kafukufukuyu ayenera kukhala athanzi, alibe HIV, komanso a zaka za pakati pa 18 ndi 35. Amayiwa akhale okonzeka kumawunikidwa umoyo wawo komanso kulandira uphungu ndi kuyezetsa HIV pafupifpafupi. Sakuyenera kukhala oyembekezera kapena woyamwitsa. Palinso zoyenereza zina zomwe ayenera kukwaniritsa kuti athe kutenga nawo mbali mu kafukufukuyu.

Zomwe munga yembekezere ngati mwasankha kutenga nawo mbali mu kafukufukuyu

Tidzakuyankhani mafunso ena alionse amene mungakhale nawo pofuna kuonetsetsa kuti mwamvetsetsa zomwe zimachitika munthu akamatenga nawo mbali mu kafukufukuyu.

  • Tidzaunika m’thupi lanu zimene zimaphatikizapo zoyesa magazi. Tidzatenga zoyesa zamagazi kuti tikayeze izi: HIV; pofuna kuona momwe chitetezo chanu cha m’thupi chimagwirira ntchito ndi katemera wa m’kafukufuku, kuyeza mwachidule zakumtundu komanso zoyeza zina zimene zingathandize ofufuza kuti amvetsetse bwino umoyo ndi chitetezo cha m’thupi cha otenga nawo mbali mukafukufuku.
  • Panthawi imene kafukufuku akuchitika, mudzapita kuclinic yya kafukufuku maulendo okwana 17 m’zaka zitatu. Pa maulendo 4 mudzalandira jakisoni wa katemera kapena wongoyerekeza. Mudzalandira majakisoni okwana 6 panthawi yonse ya kafukufuku.
  • Mudzapemphedwa kuti muzilembera za momwe mukumvera nthupi  pamasiku atatu kulekeza 7 chilandilireni jakisoni wina aliyense. Zikatha zimenezi inuyo komanso achipatala mudzakambirana kuti adziwe momwe mukumvera.
  • Maulendo ena otsatira adzakhala okalandira uphungu ndi kukayezetsa HIV komanso kuyankha mafunso kuchokera kwa ogwira ntcito ku clinic. Maulendo amenewa adzakhala aafupi kusiyana ndi maulendo amene muzikalandira jakisoni.
  • Polandira uphungu mudzalangizidwa za njira zabwino kwambiri zimene mungatsate pofuna kudziteteza ku HIV panthawi imene muli mu kafukufukuyu.

Kafukufukuyu adzachitika liti ndipo adzachitikira kuti?

Kafukufukuyu adzayamba kulemba anthu m’mwezi wa November 2017 ndipo adzachitikira m’zipatakla zingapo ku South Africa, Malawi, Mozambique, Zambia, ndi Zimbabwe.