Za Imbokodo

Imbokodo ni chiani?

Imbokodo ni  maphunziro ofufuza wamkulu uyo ayeserera makatemera yawiri yotetezera HIV. Awa makatemera ayitaniwa kuti Ad26.Mos4.HIV (Ad26 vaccine) na Clade C gp140 (protein vaccine). Zolinga zenizeni za maphunziro ofufuza ndi kufuna kuziwa ngati:

  • Awa makatemera angachinjilize HIV?
  • Awa mankhwala a katemera alibe ziopsezo ku anthu?
  • Chitetezo cha muthupi chingamenyane na makatemera ya maphunziro ofufuza?

Makatemera awo ayesedwa mu maphunziro ofufuza awa SANGAYAMBISE HIV kapena AIDS. Zinthu zomwe zasewenzesedwa mu maphunziro ofufuza awa sizinapangiwe kuchoka ku HIV yamoyo, HIV yopaiwa, kapena maselo a munthu omwe ali ndi HIV. Aya mankhwala a katemela sangapangise munthu kudwala HIV olo kapena AIDS. Zinapangiwa ku zinthu zinangu zolingana na HIV choncho sizingapereke HIV kapena AIDS.

Awa makatemera niwoyeserera chabe. Izi zitanthauza kuti akali kufufuza nakuphunzirabe ngati katemera alibe ziopsezo kapena ngati angachinjilize HIV.

Makatemara asewenzewa pa maphunziro ofufuza chabe. Siwopereka kwa anthu onse kapena kugulisa. Makatemera aperekewa na kampani iyo ipanga ya Janssen Vaccines & Prevention B.V., gawo ya Janssen Pharmaceutical Companies of Johnson & Johnson.

Nikambireni za Imbokodo

Imbokodo ni maphunziro ofufuza wamkulu uyo cholinga chake nikuonesa kuti makatemera angachinjiliza azimayi a ku sub-Saharan Africa ku kalombo ka HIV. ngati maphunziro ofufuza ya Imbokodo adzaonesa kuti athandiza azimayi, chizakhala chinthu chofunikira pa ntchito yofufuza katemera wochinjiliza anthu ku HIV paziko lonse.

Maphunziro ofufuza  yenangu ayo anachitika mu 2009, anaonesa kwa nthawi yoyamba kuti katemera angachinjiliza HIV ngakhale anasewenza pang’ono. Ayo ofufuza ayitaniwa kuti RV144 ndipo anachitika ku Thailand ndi anthu oposa 16000. Malizauti yamenewa anali osangalasa chifukwa anaonesa kuti anachinjiliza HIV na 31.2 %. Malizauti amene akuonesa kuti makatemera a mu maphunziro ofufuza ya RV144 anachinjiliza HIV kwa munthu mmodzi mu anthu atatu awo analandira katemera. maphunziro ofufuza ayo anathandiza ofufuza kupeza zizindikiro na uthenga wopangira katemera wabwino ngakhale kuti malizauti amenewa sanakwanira kupereka chilolezo cha katemera. Makatemera awo ayesewa mu maphunziro ofufuza ya Imbokodo ni yosiyana na awo anasewenzesewa mu maphunziro ofufuza ya RV144.

Makatemera awo asewenzesewa mu maphunziro ya Imbokodo na makatemera enangu, anayesewako mumaphunziro ofufuza ena ang’ono. Imozi mwa maphunziro ofufuza amenewa ndi iyo iyitaniwa kuti Approach, imene isewenzesa katemera wolingana wa Ad26 vaccine na katemera wa mapolotini ngati wa Imbokodo. maphunziro ofufuza aya achitika ku US, Rwanda, Uganda, South Africa, na ku Thailand. Makatemera ya Ad26 ni ya puloteni womwe asewenzewa mu Imbokodo apasiwa ku anthu 235 mu maphunziro ofufuza awiri ku US, Kenya, ni Rwanda awo ayitaniwa kuti HVTN 117 (Traverse) na HVTN 118 (Ascent). maphunziro ofufuza ya Ascent ali kuyamba chabe ndipo cholinga nichofuna kuona ngati makatemera ya Ad26 ni ya puloten (awo asewenzewa futi mu Imbokodo) siwabweresa mavuto pathupi ya munthu; ngati anthu angapasiwa makatemera popanda kukhalapo na mavuto; kuona momwe zipangizo za chitetezo cha thupi zimenyana na katemela wotele. Malizauti yoyamba ya maphunziro ofufuza ya Traverse, na ya maphunziro ofufuza ya Approach iyo takambapo pamwamba apa, yanonesa kuti makatemera siwabweresa mavuto aumoyo alionse futi zipangizo za chitetezo cha thupi ziyanjana ndi katemela.

Pa maphunziro ofufuza awo achitika, palibe mavuto a zaumoyo awo anayambika chifukwa cha katemera. Olo kuti kulibe pa aja anatengako mbali mumaphunziro ofufuza anakhalapo namavuto ya umoyo alionse chifukwa cha katemela wa maphunziro ofufuza, zingachitike kuti kungapezeke vuto yakuti kulibe wamene ayiyembekezela.Nchifukwa chake chimozi cha zolinga za maphunziro ofufuza aya nikupima nakuona ngati katemela alibe ziopsyezo akapasiwa ku anthu ambili.Umoyo wa munthu aliyense otengako mbali tizaunyang’anira nthawi yonse ya maphunziro ofufuza.

Imbokodo asiyana na maphunziro ofufuza ang’ono chifukwa mu Imbokodo, ofufuza afuna kuziwa ngati Katemera wa Ad26 na katemera wa puloteni angachinjilize HIV.

Ni mabungwe otani omwe achita maphunziro ofufuza?

Maphunziro ofufuza achitiwa ndi a HVTN, Janssen Vaccines & Prevention B.V., gawo ya Janssen Pharmaceutical Companies of Johnson & Johnson, na makiliniki onse awo achita nawo maphunziro ofufuza. Mabungwe awa asewenza pamodzi na anthu amudera ni cholinga chofuna kuonesesa kuti maphunziro ofufuzaniwovomerezeka ni anthu ndipo alemekeza vikhalidwe.