1. Kafukufuku wa yakatemela nichani?

Katemela ilengesa thupi kuteteza kapena kumenya matenda yenangu. Kuti mankhwala yakatemela yapangiwe, anthu akafufuku afunika kuyayesela pa anthu. Makafukufuku yenangu yakatemela yachitika kuona ngati sabwelesa mavuto pathupi ya munthu ndi kuona ngati zipangizo za chitetezo cha thupi ziyanjana ndi katemela wotele. Zipangizo za chitetezo cha thupi yanu zikutetezani ku matenda. Kafukufuku winangu aa katemela yangasewenzesedwe futi kufuna kuziwa ngati katemela ingathandize kuteteza kapena kumenya matenda. Kafukufuku wambili amachitika kuti apange katemela yoyenela komanso yamene ili na mphamvu kusewenza.

Pali ino nthawi, kulibe katemela wa mankhwala ololeka ya HIV kapena AIDS.

2. Kodi kafukufuku wa HVTN 705/HPX2008 ndi chani?

HVTN 705/HPX2008 vipimo va nambala 2 ndi vipimo vili pamuyeso womenyana ndi HIV. Mankhwal a katemela mu kafukufuku uyu aitaniwa kuti Ad26.Mos4.HIV ndi Clade C gp140. Aya mankhwala akatemela anapingiwa ndi Janssen Vaccines & Prevention B.V. Kuchoka apa, tizawaitana mankhwala kuti Ad26 ndi Protein kapena kuti mankhwala a kafukufuku.

Mankhwala akatemela a Ad26

Mankhwala a katemela a Ad26 amapangiwa kuchokela ku kalombo kamene kaitaniwa kuti Adenovirus ka mtundu wa 26. Uyu katemela ali nayo mbali ya HIV yoikiwamo. Imapangiwa mu njila yakuti imapanga mapuloteni yamene yapalana na puloteni yamene ipezeka mu HIV. (Mapuloteni ni vinthu va chilengedwe yamene yapezeka mu vinthu vonse vamoyo monga thupi ya munthu na zilombo monga HIV.) Zipangizo za thupi ya munthu yomwe imenya matenda yangachite zina zake kulingana ndi mbali zina za ma puloteni a HIV mu kafukufuku wa katemela. Iyi iitaniwa kuti kuyankha kwa zoteteza thupi. Kuyankha kwa zoteteza za thupi ilengesa thupi kuzindikila mapuloteni ofanana omwe na amene ali mu HIV ndi kumenya kalombo ngati munthu wakhala ndi HIV msogolo. Adenovirus mtundu wa 26 umapezeka kwambiri mu umoyo wa anthu ndipo ingapangise kumvela vimfine na matenda okhuza kapemedwe. Angakhale zili choncho, adenovirus yasewenzesedwa mu katemela ya kafukufuku uyu yachepesewako mphamvu kuti isabwelese matenda ndiponso ilibe ciopsyezo ku anthu.

Katemela wa Puloteni

Katemela wa puloteni, Clade C gp140, upangiwa kuchokela ku puloteni yolingana na puloteni yamene ipezeka pamwamba pa HIV. Iyi ingachose kuyankha kwa zoteteza za thupi.

Katemela wa puloteni mu kafukufuku uyu wasanganisidwa na adijuvanti yochedwa kuti Aluminum Phosphate. Adijuvant ni kanthu kamene kaikiwa ku mankhwala a katemela kuonjezelapo kuyankha kwa chitetzo cha thupi. Aluminum isewenzesewa mu mankhwala ambiri osiyanasiyana a katemela monga maknkhwala a Hepatitis A ndi B, diphtheria, ndi tetanus.

Zinthu zomwe zasewenzesedwa mu kafukufuku uyu sizinapangiwe kuchoka ku HIV yamoyo, HIV yopaiwa, kapena maselo a munthu omwe ali ndi HIV. Aya mankhwala a katemela sangapangise munthu kudwala HIV olo kapena AIDS. 

Tingakupaseni uthenga wambili pa za mankhwala a katemela a mu kafukufuku ngati mungafune.

3. Ndi mabungwe otani omwe atengako mbali mu kafukufukuyu?

A National Institute of Allergy and Infectious Diseases (NIAID), a HIV Vaccine Trials Network (HVTN) ndi Janssen Vaccines & Prevention B.V. ndiye anakonza kafukufuku uyu. Janssen Vaccines & Prevention B.V. ndiye amene aikapo za malamulo osatila ndiponso ndiye amapasa mankhwala a katemela wa mu kafukufuku. NIAID ndi mbali ya bungwe ya National Institutes of Health (NIH), yomwe ili mbali ya boma ya Amerika.

HVTN ndi mgwilizano wa anthu ozama pa sayansi, azamakafukufuku ndi anthu ena omwe asakila katemela wa HIV omwe uli wa mphamvu komanso wopanda chiopsyezo chili chonse. HVTN umalipililidwa na bungwe ya NIAID ndipo iyi kafukufuku amene amalipililidwa ndi a Bill & Melinda Gates Foundation ndi Janssen Vaccines & Prevention B.V.

4. Ni liti ndiponso nikuti kwamene kafukufukuyu uyu azachitikila?

Kafukufuku uyu ayembekezeka kuyamba kulemba aja otengako mbali mu mwezi wa October 2017. Izachitika mu madela aya:

 • Malawi: Lilongwe
 • Mozambique: Maputo
 • South Africa: Bloemfontein, Brits, Cape Town (Emavundleni, Khayelitsha, ndi Masiphumelele), Durban (Chatsworth, eThekwini, Isipingo, Tongaat ndi Verulam), Elansdoorn, Klerksdorp, Ladysmith, Mamelodi, Medunsa, Mthatha, Rustenburg, Soshanguve, Soweto (Bara ndi Kliptown), ndi Tembisa
 • Zambia: Lusaka na Ndola
 • Zimbabwe: Harare

5. Nichifukwa chani iuyu kafukufuku achitiwa?

Kafukufuku yense wa HVTN’s amasewenza kulingana ndi cholinga cha nchito yathu kuti tipeze katemela wa HIV wa mphamvu komanso wopanda chiopsyezo. Zolinga zeni zeni za kafukufuku ndi:

 • Kuyesa ngati mankhwala a katemela wa kafukufuku angateteze munthu kuti asatenge HIV
 • Kupasa uthenga wambiri pa za ubwino wa mankhwala a katemela a mukafukufuku 
 • Kutipasako ngti nzelu pa momwe mankhwla a katemela angasewenzele kuteteza munthu kutengela HIV.

6. Ni angati anthu azakhala mu kafukufukuyu, ndiponso ndi anthu otani omwe angajoine?

Kafukufuku azakhala na otengako mbali azimai okha okha okwanila 2600.

Kuti ajoine mu kafukufukuyu, azimai afunika kukhala a nthanzi labwino, azaka zokwanila pakai pa 18 ndi 35, safunika kukhala wodwala matenda a HIV. Safunika kutenga mimba kapena kunyonsha. Ziliko zina ndondomeko zomwe afunika kukwanilisa. Tizawafunsa azimai pa mbili ya umoyo wao, kupima thupi ndi kutenga magazi na, mtundo kuti vipimiwe. Tizawafunsa futi azimai pa zochita monga kugonana ndi kasewenzesedwe ka mankhwala.

7. Kodi awa mankhwala a katemela a mu kafukufuku alibe chiopsyezo?

Sitiziwa zopsyezo zonse za katemela wa kafukufuku uyu chifukwa inapasiwapo chabe ku anthu ang’ono. Katemela wa puloteni unapasiwapo ku anthu monga ngati 300 ndipo katemela wa Ad26 unapasiwapo ku anthu monga okwanila 110. Olo kuti kulibe pa aja anatengako mbali mumakafukufuku anakhalapo namavuto ya umoyo alionse chifukwa cha katemela wa kafukufuku, zingachitike kuti kungapezeka vuto yakuti kulibe wamene ayiyembekezela. Nchifukwa chake chimozi cha zolinga za kafukufuku uyu nikupima nakuona ngati katemela alibe ziiopsyezo akapasiwa ku anthu ambili. Umoyo wa munthu aliyense otengako mbali uzasamaliwa na manesi ophunzila na madokotala nthawi yonse ya kafukufuku.

8. Kodi iyi katemela ya kafukufuku ingachinjilize otengako mbali mu kafukufuku kuti asatenge HIV?

Otengako mbali asayembekeze kuchinjiliziwa ku HIV na mankhwala akatemela aya. Otengako mbali mwina sazalasiwako nyeleti ya katemela mu kafukufuku uyu chifukwa opitilila hafu anthu azatenga pulasebo. Pulasebo mu kafukufuku uyu ndi manzi amunyu.

Kafukufuku uyu yakonzewa na cholinga chofuna kuziwa ngati katemela wa mankhwala asewenza kuchinjiliza kapena kumenya HIV.

Chifukwa sitiziwa ngati katemela wa kafukufuku uyu uzasewenza kuchinjiliza anthu ku HIV/AIDS, otengako mbali mu kafukufuku uyu azapasiwa uphungu pa njila zomwe angapewelemo HIV/AIDS, ndipo azatumiwa ku malo otengelako mankhwala kwamene angapezeko njila zamopewela kutenga HIV.

9. Chizatenga nthawi itali bwanji kuziwa ngati katemela wa kafukufuku asewenza?

Tiyembekeza kuziwa ngati mankhwala a katemela a kafukufuku achinjiliza kutenga HIV mu zaka zokwanila 4. Nikotheka kuti tingaziwe mwamusanga. 

10. Kodi umoyo ndi maufulu ya otengako mbali azachinjilizidwa bwanji?

Kuchinjiliza umoyo na kulemekeza ufulu wa anthu otengako mbali ni cinthu cofunikila kwambili kwa aliyense mu HVTN na Janssen Vaccines. Popanda anthu ozipeleka, sembe sitinakwanise kupeza katemela wa HIV.

Ndondomeko yoyamba mukuchinjiliza maufulu a anthu otengako mbali mu kafukufuku ndi kuwapasa uthenga pazakafukufuku akalibe kujoina. Anyanchito a pakiliniki azapasa anthu uthenga pa zosewenzesewa mu kafukufuku na ndondomeko zake, zangozi zingapezekepo na phindu kwa otengako mbali na maufulu omwe ali nao. Ichi chiikapo ufulu wolandila uthenga wina ulionse wasopano wokhuza kafukufuku ndi zomwe zingakhuze kapena otengako mbali, ngati afuna kupitiliza kukhala mu kafukufuku ndi ufulu wochokamo mu kafukufuku pa nthawi ili yonse.

Pa nthawi ya kafukufuku, anyanchito apakiliniki azayanganila otengako mbali kusimikiza kuti katemela wa kafukufuku siubwelesa mavuto aumoyo alionse. Anyanchito apakiliniki azafunsanso otengako mbali pa zamavuto aumunthu alionse omwe angapeze chifukwa chokhala mu kafukufuku. Ngati otengako mbali ali na vuto yaumoyo kapena vuto ya zaumunthu, anyanchito akiliniki azawathandiza.

Pali magulu ambili omwe ateteza za ufulu wa otengko mbali kuikapo mkhalidwe wao:

 • Agulu loyanganila zakuti mulibe ziopsyezo mu kafukufuku, aoyanganila kuti uthenga usungidwa mosamalika amayanganila kambili kambili pauthenga wokhuza kafukufuku kuona kuti ngati chilibwino kupitiliza kupasa manyeleti/nsingano amukafukufuku.
 • Bungwe la Institutional Review Board (IRB) olo gulu ya Ethics Committee (EC) imasandasanda ndi kuyanganila ndondomeko ya kafukufuku pa kiliniki iliyonse yamene ichita kafukufuku, kuikapo uthenga wamene upasidwa ku anthu pa kafukufuku, kupita pasogolo kwa kafukufuku, ndi mavuto okhuza umoyo kwa otengako mbali mu kafukufuku. Bungwe la IRB/EC imayangananso kuona ngati maufulu a otengako mbali alemekezeka.
 • Bungwe la South Africa Medicines Control Council,kuzanso a national regulatory authorities akuvyalo kwinangu, amayanganila momwe kafukufuku ichitikila ndiponso amafuna kulandila mbili pa zaufulu ndi mtendere wa otengako mbali.
 • Abungwe la US Food & Drug Administration (FDA) naonso amayanganila kafukufuku uyu. Bungwe la FDA imaona kuti malamulo a amerika okhuza kafukufuku oonkhewa pa anthu ndi kasewenzesedwe ka katemela mu kafukufuku.
 • Kiliniki iliyonse ili na gulu lochedwa Institutional Biosafety Committee (IBC) yamene imayanganila mwamene nyeleti za katemela zikonzedwa mu famasi na mwamene visewenzesewa mu kiliniki.
 • Makiliniki ena ali nayo gulu lapadela lochedwa special Ethics Committees yamene iyanganila malo kwamene magazi na zosewenzesa zinangu zisungiwila. Aya malo amayaitana kuti bio-banks kapena kuti malo osungilamo zinthu.
 • Cigao coyanganila ulimi, zamthengo ndi za nsomba laku south Africa lochedwa South Africa Department of Agriculture, Forestry, and Fisheries (DAFF) iyi ni gulu ya anthu apadela yamene ifunika kuyanganila ndo kuvomekeza onse makalata opempha kuti abwelese mu chalo zinthu zomwe zimakula ndi mankhwala kapena kuti genetically modified materials (GMO) monga katemela wa mtundu wa Ad26 mu kafukufuku uyu. 
 • Kiliniki iliyonse ili na gulu ya aphungu ochedwa Community Advisory Board (CAB). Ma membala ake ndi nzika kapena kuti eni ake malo omwe abwelesa zakumutima kapena zofuna za anthu akwamene mukhala kuzanso aja amene atengako mbali mu phnzilo. Ma membala a CAB ali mbali ya gulu yamene inakonza kafukufuku uyu. Amathandizanso kupanga kapena kusandasanda uthenga wamene upasiwa kwa otengako mbali.

11. Kodi katemela uyu ungalengese munthu kuoneka kuti ali na HIV ngati apimiwa HIV?

Inde, katemela wa kafukufuku ungalengese anthu ena kunkhala namalizauti oonesa kuti ali na HIV ngati wamipiwa pa vipimo vinanguvinangu va HIV. Ngati otengako mbali atenga katemela wa HIV, thupi lao lingapange mphamvu yamene imenya matenda mthupi omwe achedwa kuti antibodizi muchizungu. Ma antibodizi yamathandiza kumenya matenda muthupi. Vipimo vambili va HIV vimasakila ma antibodizi ya HIV kukhala ngati chisonyezo kuti uli na matenda. Chifukwa cha ichi, munthu angapezeke kuti ali na HIV olo kuti alibe matenda ya HIV. Ichi chiitaniwa kuti vaccine-induced seropositive (VISP) kuthanthauza kuti chipimo ndiye chalengesa kuti uli na HIV chifukwa cha katemela. Iyi iitaniwa futi ati vaccine-Induced Seroreactivity (VISR). Sitiziwa amene azakhala na malizauti yotele futi sitiziwa kuti aya malizauti yangakhale choncho kwa nthawi yaitali bwanji.

Anthu amene apezeka na malizauti ya VISP afunika chipimo cheni cheni cha HIV kusimikiza kuti lizauti iyi nichifukwa cha katemela olo kapena ni chifukwa cha kudwala HIV kwazoona. Makiliniki amene atengako mbali mu kafukufuku ali nayo danga yotenga vipimo venevene vamene vionesa kalombo ka HIV osati chabe ma antibodizi. Anthu otengko mbali mu katemela wa kafukufuku afunika kupimiwa chabe pa makiliniki amene atengako mbali mu kafukufuku uyu. 

Kulibe mavuto aumoyo amene azabwela chifukwa cha HIV lizauti yamene yapangiwa na katemela kapena kuti VISP, koma lizauti ya VISP ingalengese mavuto mu mbali zina zambili monga za mankhwala olo kasungidwe ka menu, kulembewa nchito, inshuwalansi, chitupa choyendela ku vyalo vinangu kapena kuti viza olo kulowa usilikali. Anthu sangalolewe kupasa magazi kapena ziwalo zina zili zonse. Ngati otengako mbali afuna kupata inshuwalansi, kolowa nchito, kapena usilikali afunika kuuza omwe achitisa kafukufuku ku dela lakwao mwamusanga. Kampani ya inshuwalansi, kampani yamene ilemba nchito, kapena chigao cha asilikali sangavomela malizauti ya HIV yochokela ku HVTN. Angakhale zili choncho, a gulu ya HVTN angasewenzele nao pamozi kuona kuti chipimo chenicheni cha HIV chachitika chamene chingaonese malizauti yazoona. Ngati muli na ma antibodizi aya elo mwankhala na mimba, yangamuyambukile mwana, angapimiwe nooneka molakwika kuti ali na HIV noikiwa pa mankhwala. Kiliniki yamene ichita kafukufuku ingakupaseni pepala ya malizauti yanu kuti musewenzese kuli konse kwamene mufuna.

12. Kodi ningaupeze kuti uthenga wambili pa nkhani iyi?

Zokhuza katemela wa makafukufuku a mumakiliniki: www.clinicaltrials.gov

Zokhuza netiweki ya kuyeyesa kwa katemela wa HIV: www.hvtn.org

Zokhuza VISP: http://www.hvtn.org/VISP

Ngati muli nao mafunso yenangu yamene sanayankhidwe mu pepala iyi, chonde tifunseni. Mungatumile: [email protected]