Wotengako Mbali

Ni angati anthu azakhala mu maphunziro ofufuza, ndiponso ndi anthu otani angajoine?

Aya maphunziro ofufuza azakhala ni azimayi otengako mbali 2600 a ku South Africa, Malawi, Mozambique, Zambia, ndi Zimbabwe. Kuti ajoine mu maphunziro ofufuza aya, azimayi afunika kukhala wathanzi labwino, azaka zokwanila pakati pa 18 ndi 35, safunika kukhala na HIV. Azimayi awa ayenera kukhala okonzeka kupimiwa thupi ndi kupasiwa malangizo ndi kupimiwa HIV. Safunika kutenga mimba kapena kunyonsha Ziliko zina ndondomeko zomwe afunika kukwanilisa kuti ajoine mu maphunziro ofufuza.

Mungayembekeze chiani ngati mwajoina maphunziro ofufuza

Tizayankha mafunso yonse awo muli nawo kuti mumvesese zomwe zichitika ngati mwatenga mbali mu maphunziro ofufuza.

  • Muzapimiwa thupi kuikapo futi magazi. Magazi tizawasewenzesa pofuna: kupima ngati muli na HIV; kuona umo chitetezo cha muthupi chisewenzera pomenyana na mankhwala ya katemnera wa maphunziro yofufuza; pang’ono tizapima umo thupi lanu linapangiwira na vipimo vinangu ivo vizathandiza ofufuza kumvesa bwino za umoyo wa otenga mbali na chitetezo cha thupi lawo.
  • Pa nthawi yonse ya maphunziro ofufuza muzayenda ku kiliniki maulendo 17 mu zaka zitatu. Pa maulendo yatatu muzapasiwa nyeleti ya katemera wa maphunziro kapena pulasebo. Zonse pamozi muzapasiwa manyeleti 6 pa nthawi yonse ya maphunziro ofufuza.
  • Muzafunsiwa kulemba momwe mumvera mu thupi mwanu kwa masiku 3 mpaka 7 kuchokera pamene mwapasiwa nyeleti. Ikapita nthai iyi, inu ndi antchito a maphunziro ofufuza muzakambirana kufuna kuona momwe mumvelera mu thupi lanu.
  • Maulendo enangu oyenda ku kiliniki muzalandira ulangizi wa HIV ndi kupiwa HIV, futi azayankha mafunso antchito amaphunziro. Aya maulendo azatenga nthawi yochepa kusiyana na maulendo enangu.
  • Alangizi a HIV azakupasani malangizo othandiza kuti muzichinjilize ku HIV panthawi yomwe mutenga nawo mbali mu maphunziro ofufuza.

Ni liti ndiponso nikuti kwamene maphunziro ofufuza azachitika?

Maphunziro ofufuza aya ayembekezeka kuyamba kulemba aja otengako mbali mu mwezi wa November 2017 ndipo yazachitika mu madela ambiri ku South Africa, Malawi, Mozambique, Zambia, ndi Zimbabwe.